1. Imvani Yehova, mau anga, m'kudandaula kwanga;Sungani moyo wanga angandiopse mdani.
2. Ndibiseni pa upo wacinsinsi wa ocita zoipa;Pa phokoso la ocita zopanda pace:
3. Amene anola lilime lao ngati lupanga,Napiringidza mibvi yao, ndiyo mau akuwawitsa;
4. Kuponyera wangwiro mobisika:Amponyera modzidzimutsa, osaopa.
5. Alimbikitsana m'cinthu coipa;Apangana za kuchera misampha mobisika;Akuti, Adzaiona ndani?
6. Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi kutha;Cingakhale ca m'kati mwace mwa munthu, ndi mtima wozama.
7. Koma Mulungu adzawaponyera mubvi;Adzalaswa modzidzimutsa,
8. Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;Onse akuwaona adzawathawa.
9. Ndipo anthu onse adzacita mantha;Nadzabukitsa cocita Mulungu,Nadzasamalira nchito yace.
10. Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye;Ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.