1. Mulungu adziwika mwa Yuda:Dzina lace limveka mwa Israyeli.
2. Msasa wace unali m'Salemu, Ndipo pokhala Iye m'Ziyoni.
3. Pomwepo anatyola mibvi ya paota;Cikopa, ndi lupanga, ndi nkhondo.
4. Inu ndinu wakuunikira, ndi womveka wakuposa mapiri muli acifwamba.
5. Olimba mtima cifunkhidwa cuma cao, agona tulo tao;Amuna onse amphamvu asowa manja ao.
6. Pa kudzudzula kwanu, Mulungu wa Yakobo,Gareta ndi kavalo yemwe anagwa m'tulo.
7. Inu ndinu woopsa;Ndipo utauka mkwiyo wanu adzakhala ciriri ndani pamaso panu?
8. Mudamveketsa ciweruzo cocokera Kumwamba;Dziko lapansi linacita mantha, nilinakhala cete,
9. Pakuuka Mulungu kuti aweruze,Kuti apulumutse ofatsa onse a pa dziko lapansi.
10. Indedi, kuzaza kwace kwa munthu kudzakulemekezani;Cotsalira ca kuzazaku mudzaciletsa.
11. Windani ndipo citirani Yehova Mulungu wanu zowindazo;Onse akumzinga abwere naco copereka ca kwa Iye amene ayenera kumuopa.
12. Iye adzadula mzimu wa akulu;Akhala woopsa kwa mafumu a pa dziko lapansi.