1. Yehova, mtima wanga sunadzikuzaNdi maso anga sanakwezeka;Ndipo sindinatsata zazikuru,Kapena zodabwiza zondiposa.
2. Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga;Ngati mwana womletsa kuyamwa amace,Moyo wanga ndiri nao ngati mwana womletsa kuyamwa.
3. Israyeli, uyembekezere Yehova,Kuyambira tsopano kufikira kosatha.