1. Haleluya,Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano,Ndi cilemekezo cace mu msonkhano wa okondedwa ace.
2. Akondwere Israyeli mwa Iye amene anamlenga;Ana a Ziyoni asekere mwa Mfumu yao.
3. Alemekeze dzina lace ndi kuthira mang'ombe;Amyimbire zomlemekeza ndi lingaka ndi zeze.
4. Popeza Yehova akondwera nao anthu ace;Adzakometsa ofatsa ndi cipulumutso,
5. Okondedwa ace atumphe mokondwera m'ulemu:Apfuule mokondwera pamakama pao,
6. Nyimbo zakukweza Mulungu zikhale pakamwa pao,Ndi lupanga lakuthwa konse konse m'dzanja lao;
7. Kubwezera cilango akunja,Ndi kulanga mitundu ya anthu;
8. Kumanga mafumu ao ndi maunyolo,Ndi omveka ao ndi majerejede acitsulo;
9. Kuwacitira ciweruzo colembedwaco:Ulemu wa okondedwa ace onse ndi uwu.Haleluya.