1. Citsiru cimati mumtima mwace, Kulibe Mulungu.Acita zobvunda, acita cosalungama conyansa;Kulibe wakucita bwino.
2. Mulungu m'mwamba anaweramira pa ana a anthu,Kuti aone ngati aliko wanzeru, Wakufuna Mulungu.
3. Onse anabwerera; anabvunda mtima pamodzi;Palibe mmodzi wakucita bwino, nnena mmodzi.
4. Kodi ocita zopanda pace sadziwa?Pomadya anthu anga monga akudya mkate;Ndipo saitana Mulungu.
5. Pamenepo anaopa kwakukuru, popanda cifukwa ca kuopa:Pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe;Unawacititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.
6. Ha, cipulumutso ca Israyeli cicokere m'Ziyoni!Pakubweretsa Mulungu anthu ace a m'ndende,Yakobo adzakondwera, Israyeli adzasekera.