1. Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,Ndipo musandilange m'ukali wanu.
2. Mundicitire cifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine:Mundicize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
3. Moyo wanganso wanthunthumira kwakukuru;Ndipo Inu, Yehova, kufikira liti?
4. Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga;Ndipulumutseni cifukwa ca kukoma mtima kwanu.
5. Pakuti muimfa m'mosakumbukila Inu:M'mandamo adzakuyamikani dani?
6. Ndalema nako kuusa moyo kwanga;Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse;Mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.
7. Lapuwala diso langa cifukwa ca cisoni;Lakalamba cifukwa ca onse akundisautsa.
8. Cokani kwa ine, nonsenu akucita zopanda pace;Pakuti wamva Yehova mau a kulira kwanaa,
9. Wamva Yehova kupemba kwanga;Yehova adzalandira pemphero langa.
10. Adzacita manyazi, nadzanthunthumira kwakukuru adani anga onse;Adzabwerera, nadzacita manyazi modzidzimuka,