1. Yehova akubvomereze tsiku la nsautso;Dzina la Mulungu wa Yakobo likuike pamsanje;
2. Likutumizire thandizo loturuka m'malo oyera,Ndipo likugwirizize kucokera m'Ziyoni;
3. Likumbukile zopereka zako zonse,Lilandire nsembe yako yopsereza;
4. Likupatse ca mtima wako,Ndipo likwaniritse upo wako wonse.
5. Tidzapfuula mokondwera mwa cipulumutso canu,Ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera:Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
6. Tsopano ndidziwa kuti Yehova apulumutsa wodzozedwa wace;Adzambvomereza m'Mwamba mwace moyeraNdi mphamvu ya cipulumutso ca dzanja lace lamanja.
7. Ena atama magareca, ndi ena akavalo:Koma ife tidzachula dzina la Yehova Mulungu wathu.
8. Iwowa anagonieka, nagwa:Koma ife tauka, ndipo takhala ciriri.
9. Yehova, pulumutsani,Mfumuyo atibvomereze tsiku lakuitana ife.