1. Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano;Myimbireni Yehova, inu, dziko lonse lapansi.
2. Myimbireni Yehova, lemekezani dzina lace;Lalikirani cipulumutso cace tsiku ndi tsiku.
3. Fotokozerani ulemerero wace mwa amitundu;Zodabwiza zace mwa mitundu yonse ya anthu.
4. Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;Ayenera amuope koposa milungu yonse.
5. Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano:Koma Yehova analenga zakumwamba.
6. Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu:M'malo opatulika mwace muli mphamvu ndi zocititsa kaso.
7. Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu,Mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu,
8. Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lace;Bwerani naco copereka, ndipo fikani ku mabwalo ace.
9. Gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa:Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi.
10. Nenani mwa amitundu, Yehova acita ufumu;Dziko lokhalamo anthu lomwe likhazikika kuti silingagwedezeke;Adzaweruza mitundu ya anthu molunjika.
11. Kumwamba kukondwere nilisekerere dziko lapansi;Nyanja ibume mwa kudzala kwace:
12. Munda ukondwerere ndi zonse ziri m'mwemo;Pamenepo mitengo yonse ya kunkhalango idzapfuula mokondwera;
13. Pamaso pa Yehova, pakuti akudza;Pakuti akudza kudzaweruza dziko lapansi:Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi cilungamo,Ndi mitundu ya anthu ndi coonadi.