1. Ndipulumutseni, Mulungu, mwa dzina lanu,Ndipo mundiweruze ndi mphamvuyanu.
2. Imvani pemphero langa, Mulungu;Cherani khutu mau a pakamwa panga.
3. Pakuti alendo andiukira,Ndipo oopsa afunafuna moyo wanga;Sadziikira Mulungu pamaso pao.
4. Taonani, Mulungu ndiye mthandizi wanga:Ambuye ndiye wacirikiza moyo wanga.
5. Adzabwezera coipa adani anga:Aduleni m'coonadi canu.
6. Ine mwini ndidzapereka nsembe kwa Inu:Ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.
7. Pakuti anandilanditsa m'nsautso yonse;Ndipo ndapenya ndi diso langa ico ndakhumbira pa adani anga,