1. Anandisautsa kawiri kawiri kuyambira ubwana wanga,Anene tsono Israyeli;
2. Anandisautsa kawiri kawiri kuyambira ubwana wanga;Koma sanandilaka.
3. Olima analima pamsana panga;Anatalikitsa mipere yao.
4. Yehova ndiye wolungama;Anadulatu zingwe za oipa.
5. Acite manyazi nabwerere m'mbuyo.Onse akudana naye Ziyoni.
6. Akhale ngati udzu womera patsindwi,Wakufota asanauzule;
7. Umene womweta sadzaza nao dzanja lace,Kapena womanga mitolo sakupatira manja.
8. Angakhale opitirirapo sanena,Dalitso la Mulungu likhale pa inu;Tikudalitsani m'dzina la Yehova.