1. Aticitire cifundo Mulungu, ndi kutidalitsa,Atiwalitsire nkhope yace;
2. Kuti njira yanu idziwike pa dziko lapansi,Cipulumutso canu mwa amitundu onse.
3. Anthu akuyamikeni, Mulungu;Anthu onse akuyamikeni.
4. Anthu akondwere, napfuule makondwera;Pakuti mudzaweruza anthu malunjika,Ndipo mudzalangiza anthu pa dziko lapansi.
5. Anthu akuyamikeni, Mulungu;Anthu onse akuyamikeni.
6. Dziko lapansi lapereka zipatso zace:Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.
7. Mulungu adzatidalitsa;Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa Iye,