1. Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu,Thandizo lopezekeratu m'masautso.
2. Cifukwa cace sitidzacita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi,Angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja;
3. Cinkana madzi ace akokoma, nacita thobvu,Nagwedezeka mapiri ndi kudzala kwace.
4. Pali mtsinje, ngalande zace zidzakondweretsa mudzi wa Mulungu.Malo oyera okhalamo Wam'mwambamwamba,
5. Mulungu ali m'kati mwace, sudzasunthika:Mulungu adzauthandiza mbanda kuca.
6. Amitundu anapokosera; maufumu anagwedezeka:Ananena mau, dziko lapansi linasungunuka.
7. Yehova wa makamu ali ndi ife;Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.
8. Idzani, penyani nchito za Yehova,Amene acita zopululutsa pa dziko lapansi.
9. Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi;Athyola uta, nadula nthungo;Atentha magareta ndi moto.
10. Khalani cete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu:Ndidzabuka mwa amitundu,Ndidzabuka pa dziko lapansi.
11. Yehova wa makamu ali ndi ife,Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu,