1. Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino:Pakuti cifundo cace ncosatha.
2. Yamikani Mulungu wa milungu:Pakuti cifundo cace ncosatha.
3. Yamikani Mbuye wa ambuye:Pakuti cifundo cace ncosatha.
4. Amene yekha acita zodabwiza zazikuru:Pakuti cifundo cace ncosatha.
5. Amene analenga zakumwamba mwanzeru:Pakuti cifundo cace ncosatha.
6. Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi:Pakuti cifundo cace ncosatha.
7. Amene analenga miuni yaikuru:Pakuti cifundo cace ncosatha.
8. Dzuwa liweruze usana:Pakuti cifundo cace ncosatha.
9. Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku;Pakuti cifundo cace ncosatha.
10. Iye amene anapandira Aaigupto ana ao oyamba:Pakuti cifundo cace ncosatha.
11. Naturutsa Israyeli pakati pao;Pakuti cifundo cace ncosatha.
12. Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka:Pakuti cifundo cace ncosatha.
13. Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira:Pakuti cifundo cace ncosatha.
14. Napititsa Israyeli pakati pace;Pakuti cifundo cace ncosatha.
15. Nakhutula Farao ndi khamu lace m'Nyanja Yofiira:Pakuti cifundo cace ncosatha.
16. Amene anatsogolera anthu ace m'cipululu:Pakuti cifundo cace ncosatha.
17. Amene anapanda mafumu akulu:Pakuti cifundo cace ncosatha,
18. Ndipo anawapha mafumu omveka:Pakuti cifundo cace ncosatha.
19. Sihoni mfumu ya Aamori;Pakuti cifundo cace ncosatha.
20. Ndi ogi mfumu ya Basana:Pakuti cifundo cace ncosatha.
21. Ndipo anaperekadzikolaolikhale cosiyira;Pakuti cifundo cace ncosatha.
22. Cosiyira ca kwa Israyeli mtumiki wace;Pakuti cifundo cace ncosatha.
23. Amene anatikumbukila popepuka ife;Pakuti cifundo cace ncosatha.
24. Natikwatula kwa otisautsa;Pakuti cifundo cace ncosatha.
25. Ndiye wakupatsa nyama zonse cakudya;Pakuti cifundo cace ncosatha.
26. Yamikani Mulungu wa kumwamba,Pakuti cifundo cace ncosatha.