1. Myimbireni Yehova nyimbo yatsopano;Popeza anacita zodabwiza:Dzanja lace lamanja, mkono wace woyera, zinamcitira cipulumutso,
2. Yehova anawadziwitsira cipulumutso cace;Anaonetsera cilungamo cace pamaso pa amitundu.
3. Anakumbukila cifundo cace ndi cikhulupiriko cace ku nyumba ya Israyeli;Malekezero onse a dziko lapansi anaona cipulumutso ca Mulungu wathu.
4. Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi;Kuwitsani ndi kupfuulira mokondwera; inde, yimbirani zomlemekeza.
5. Myimbireni Yehova zomlemekeza ndizeze;Ndi zeze ndi mau a salmo.
6. Pfuulani pamaso pa Mfumu Yehova,Ndi mbetete ndi liu la lipenga,
7. Nyanja Ipfuule ndi kudzala kwace;Dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhalamo;
8. Mitsinje iombe manja;Mapiri apfuule pamodzi mokondwera;
9. Pamaso pa Yehova, popeza akudza kudzaweruza dziko lapansi;Adzaweruza dziko lokhalamo anthu ndi cilungamo,Ndi mitundu ya anthu molunjika,