1. Mulungu musakhale cete;Musakhale du, osanena kanthu, Mulungu.
2. Pakuti taonani, adani anu aphokosera:Ndipo okwiyira Inu aweramutsa mutu,
3. Apangana mocenjerera pa anthu anu,Nakhalira upo pa obisika anu.
4. Amati, Tiyeni tiwaononge asakhalenso mtundu wa anthu;Ndipo dzina la Israyeli lisakumbukikenso.
5. Pakuti anakhalira upo ndi mtima umodzi;Anacita cipangano ca pa Inu:
6. Mahema a Edomu ndi a Aismayeli;Moabu ndi Ahagara;
7. Gebala ndi Amoni ndi Amaleki;Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala m'Turo.
8. Asuri anaphatikana nao;Anakhala dzanja la ana a Loti,
9. Muwacitire monga munacitira Midyani;Ndi Sisera, ndi Jabini ku mtsinje wa Kisoni:
10. Amene anaonongeka ku Endoro;Anakhala ngati ndowe ya kumunda.
11. Muwaike akulu ao ngati Orebu ndi Zeebu;Mafumu ao ngati Zeba ndi Zalimuna:
12. Amene anati, TilandeMalo okhalamo Mulungu, akhale athu.
13. Mulungu wanga, muwaike akhale ngati mungu;Ngati ziputu zomka ndi mphepo.
14. Monga moto upsereza nkhalango,Ndi monga lawi liyatsa mapiri;
15. Momwemo muwatsate ndi namondwe,Nimuwaopse ndi kabvumvulu wanu.
16. Acititseni manyazi pankhope pao;Kuti afune dzina lanu, Yehova.
17. Acite manyazi, naopsedwe kosatha;Ndipo asokonezeke, naonongeke:
18. Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova,Ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.