1. Kodi muli cete ndithu poyenera inu kunena zolungama?Muweruza ana a anthu molunjika kodi?
2. Inde, mumtima mucita zosalungama;Pa dziko lapansi mugawira anthu ciwawa ca m'manja mwanu.
3. Oipa acita cilendo cibadwire:Asokera kuyambira kubadwa kwao, nanena bodza.
4. Ululu wao ukunga wa njoka;Akunga mphiri yogontha m'khutu, itseka m'khutu mwace.
5. Imene simvera liu la oitana,Akucita matsenga mocenieratu,
6. Tyolani mano ao m'kamwa mwao, Mulungu:Zulani zitsakano za misona ya mkango, Yehova.
7. Apitetu ngati madzi oyenda;Popiringidza mibvi yace ikhale yodukaduka.
8. Apite ngati nkhono yosungunuka;Asaone dzuwa monga mtayo,
9. Miphika yanu isanagwire moto waminga,Adzaiuluza, yaiwisi ndi yoyaka.
10. Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera cilango:Adzasamba mapazi ace m'mwazi wa woipa.
11. Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama;Indedi, pali Mulungu wakuweruza pa dziko lapansi.