1. Usabvutike mtima cifukwa ca ocita zoipa,Usacite nsanje cifukwa ca ocita cosalungama.
2. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu,Ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
3. Khulupirira Yehova, ndipo cita cokoma;Khala m'dziko, ndipo tsata coonadi.
4. Udzikondweretsenso mwa Yehova;Ndipo iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.
5. Pereka njira yako kwa Yehova; Khulupiriranso Iye, adzacicita.
6. Ndipo adzaonetsa cilungamo cako monga kuunika,Ndi kuweruza kwako monga usana.
7. Khala cete mwa Yehova, numlindirire Iye:Usabvutike mtima cifukwa ca iye wolemerera m'njira yace,Cifukwa ca munthu wakucita ciwembu.
8. Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo:Usabvutike mtima ungacite coipa,
9. Pakuti ocita zoipa adzadulidwa:Koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.
10. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti:Inde, udzayang'anira mbuto yace, nudzapeza palibe.
11. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi;Nadzakondwera nao mtendere wocuruka.
12. Woipa apangira ciwembu wolungama,Namkukutira mano.
13. Ambuye adzamseka:Popeza apenya kuti tsiku lace likudza.
14. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao;Alikhe ozunzika ndi aumphawi,Aphe amene ali oongoka m'njira:
15. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe,Ndipo mauta ao adzatyoledwa.
16. Zocepa zace za wolungama zikomaKoposa kucuruka kwao kwa oipa ambiri.
17. Pakuti manja a oipa adzatyoledwa:Koma Yehova acirikiza olungama.
18. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro:Ndipo cosiyira cao cidzakhala cosatha.
19. Sadzacita manyazi m'nyengo yoipa:Ndipo m'masiku a njala adzakhuta.
20. Pakuti oipa adzatayika,Ndipo adani ace a Yehova adzanga mafuta a ana a nkhosa:Adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.
21. Woipa akongola, wosabweza:Koma wolungama acitira cifundo, napereka.
22. Pakuti iwo amene awadalitsa adzalandira dziko lapansi;Koma iwo amene awatemberera adzadulidwa.
23. Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu;Ndipo akondwera nayo njira yace.
24. Angakhale akagwa, satayikiratu:Pakuti Yehova agwira dzanja lace.
25. Ndinali mwana ndipo ndakalamba:Ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa,Kapena mbumba zace zirinkupempha cakudya.
26. Tsiku lonse acitira cifundo, nakongoletsa;Ndipo mbumba zace zidalitsidwa.
27. Siyana naco coipa, nucite cokoma,Nukhale nthawi zonse.
28. Pakuti Yehova akonda ciweruzo,Ndipo sataya okondedwa ace:Asungika kosatha:Koma adzadula mbumba za oipa.
29. Olungama adzalandira dziko lapansi,Nadzakhala momwemo kosatha.
30. Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru,Ndi lilime lace linena ciweruzo.
31. Malamulo a Mulungu wace ali mumtima mwace;Pakuyenda pace sadzaterereka.
32. Woipa aunguza wolungama,Nafuna kumupha.
33. Yehova sadzamsiya m'dzanja lace:Ndipo sadzamtsutsa poweruzidwa iye.
34. Yembekeza Yehova, nusunge njira yace,Ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko:Pakudutidwa oipa udzapenya,
35. Ndapenya woipa, alikuopsa,Natasa monga mtengo wauwisi wanzika.
36. Koma anapita ndipo taona, kwati zi:Ndipo ndinampwaira osampeza.
37. Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima!Pakuti ku matsiriziro ace a munthuyo kuti mtendere.
38. Koma olakwa adzaonongeka pamodzi:Matsiriziro a oipa adzadutidwa.
39. Koma cipulumutso ca olungama cidzera kwa Yehova,Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso.
40. Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa:Awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa,Cifukwa kuti anamkhulupirira Iye,