1. Pfuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.
2. Tumikirani Yehova ndi cikondwerero:Idzani pamaso pace ndi kumyimbira mokondwera,
3. Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu;Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ace;Ndife anthu ace ndi nkhosa za pabusa pace.
4. Lowani ku zipata zace ndi ciyamiko,Ndi ku mabwalo ace ndi cilemekezo:Myamikeni; lilemekezeni dzina lace.
5. Pakuti Yehova ndiye wabwino; cifundo cace cimamka muyaya;Ndi cikhulupiriko cace ku mibadwo mibadwo.