1. Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;
2. Amene adzipanga zoipa mumtima mwao;Masiku onse amemeza nkhondo.
3. Anola lilime lao ngati njoka;Pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.
4. Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa;Ndisungeni kwa munthu waciwawa;Kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.
5. Odzikuzaanandichera msampha, nandibisira zingwe;Anacha ukonde m'mphepete mwa njira;Anandichera makwekwe.
6. Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;Mundicherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.
7. Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya cipulumutso canga,Munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.
8. Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;Musamthandize zodzipanga zace; angadzikuze.
9. Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,Coipa ca milomo yao ciwaphimbe.
10. Makala amoto awagwere;Aponyedwe kumoto;M'maenje ozama, kuti asaukenso.
11. Munthu wamlomo sadzakhazikika pa dziko lapansi;Coipa cidzamsaka munthu waciwawa kuti cimgwetse.
12. Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,Ndi kuweruzira aumphawi,
13. Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;Oongoka mtima adzakhala pamaso panu,