1. Patsani mfumu maweruzo anu, Mulungu,Ndi mwana wa mfumu cilungamo canu.
2. Potero adzanenera anthu anu mlandu ndi m'cilungamo,Ndi ozunzika anu ndi m'ciweruzo.
3. Mapiri adzatengera anthu mtendere,Timapiri tomwe, m'cilungamo.
4. Adzaweruza ozunzika a mwa anthu,Adzapulumutsa ana aumphawi,Nadzaphwanya wosautsa.
5. Adzakuopani momwe likhalira dzuwa ndi mwezi,Kufikira mibadwo mibadwo.
6. Adzanga mvula yakugwa pa udzu wosenga:Monga mvula yothirira dziko.
7. Masiku ace wolungama adzakhazikika;Ndi mtendere wocuruka, kufikira sipadzakhala mwezi.
8. Ndipo adzacita ufumu kucokera kunyanja kufikira kunyanja,Ndi kucokera ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko lapansi.
9. Okhala m'cipululu adzagwadira pamaso pace;Ndi adani ace adzaluma nthaka.
10. Mafumu a ku Tarisi ndi ku Zisumbuzo adzabwera naco copereka;Mafumu a ku Sheba ndi Seba adzadza nazo mphatso,
11. Inde mafumu onse adzamgwadira iye:Amitundu onse adzamtumikira.
12. Pakuti adzapulumutsa waumphawi wopfuulayo;Ndi wozunzika amene alibe mthandizi.
13. Adzacitira nsoni wosauka ndi waumphawi,Nadzapulumutsa moyo wa aumphawi,
14. Adzaombola moyo wao ku cinyengo ndi ciwawa;Ndipo mwazi wao udzakhala wa mtengo pamaso pace:
15. Ndipo iye adzakhala ndi moyo; ndipo adzampatsa golidi wa ku Sheba;Nadzampempherera kosalekeza;Adzamlemekeza tsiku lonse.
16. M'dzikomo mudzakhala dzinthu dzocuruka pamwamba pa mapiri;Zipatso zace zidzati waa, ngati za ku Lebano:Ndipo iwo a m'mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.
17. Dzina lace lidzakhala kosatha:Momwe likhalira dzuwa dzina lace lidzamvekera zidzukulu:Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye;Amitundu onse adzamucha wodala.
18. Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israyeli,Amene acita zodabwiza yekhayo:
19. Ndipo dzina lace la ulemerero lidalitsike kosatha;Ndipo dziko lonse lapansi lidzale nao ulemerero wace.Amen, ndi Amen.
20. Mapemphero a Davide mwana wa Jese atha.