1. Moyo wanga ukhalira cete Mulungu yekha:Cipulumutso canga cifuma kwa Iye.
2. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi cipulumutso canga;Msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukuru.
3. Mudzambvumbvulukira munthu mpaka liti,Kumupha iye, nonsenu,Monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
4. Komatu amkhaliraupo kuti amkankhire pansi ulemu wace;Akondwera nao mabodza;Adalitsa ndi m'kamwa mwao, Koma atemberera mumtima.
5. Moyo wanga, ukhalire cete Mulungu yekha;Pakuti ciyembekezo canga cifuma kwa Iye,
6. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi cipulumutso canga,Msanje wanga, sindidzagwedezeka.
7. Pa Mulungu pali cipulumutso canga ndi ulemerero wanga:Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.
8. Khulupirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu:Tsanulirani mitima yanu pamaso pace:Mulungu ndiye pothawirapo ife.
9. Indetu, anthu acabe ndi mpweya, ndipo anthu akuru ndi bodza:Pakuwayesa apepuka;Onse pamodzi apepuka koposa mpweya,
10. Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama cifwamba;Cikacuruka cuma musakhazikepo mitima yanu.
11. Mulungu ananena kamodzi, ndinacimva kawiri:Kuti mphamvu ndi yace ya Mulungu:
12. Cifundonso ndi canu, Ambuye:Cifukwa Inu musudzula munthu ali yense monga mwa nchito yace.