Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48
  49. 49
  50. 50
  51. 51
  52. 52
  53. 53
  54. 54
  55. 55
  56. 56
  57. 57
  58. 58
  59. 59
  60. 60
  61. 61
  62. 62
  63. 63
  64. 64
  65. 65
  66. 66

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Galamuka galamuka, tabvala mphamvu zako, Ziyoni; tabvala zobvala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.

2. Dzisanse pfumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.

3. Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa cabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama.

4. Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Aigupto poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asuri anawatsendereza popanda cifukwa.

5. Cifukwa cace kodi ndicitenji pano? ati Yehova; popeza anthu anga acotsedwa popanda kanthu? akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa licitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.

6. Cifukwa cace anthu anga adzadziwa dzina langa; cifukwa cacersiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.

7. Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa cipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.

8. Mau a alonda ako! akweza mau, ayimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.

9. Kondwani zolimba, yimbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, waombola Yerusalemu.

10. Yehova wabvula mkono wace woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona cipulumutso ca Mulungu wathu.

11. Cokani inu, cokani inu, turukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; turukani pakati pace, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.

12. Pakuti simudzacoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israyeli adzadikira pambuyo panu.

13. Taonani, Mtumiki wanga adzacita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.

14. Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israyeli, momwemo nkhope yace yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ace kupambana ana a anthu;

15. momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti cimene sicinauzidwa kwa iwo adzaciona, ndi cimene iwo sanamva adzazindikira.