Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48
  49. 49
  50. 50
  51. 51
  52. 52
  53. 53
  54. 54
  55. 55
  56. 56
  57. 57
  58. 58
  59. 59
  60. 60
  61. 61
  62. 62
  63. 63
  64. 64
  65. 65
  66. 66

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 56 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Malonjezo a kwa iwo osunga Sabata

1. Atero Yehova, Sungani inu ciweruziro, ndi kucita cilungamo; pakuti cipulumutso canga ciri pafupi kudza, ndi cilungamo canga ciri pafupi kuti cib zumbulutsidwe,

2. Wodala munthu amene acita ici, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ici, amene asunga sabata osaliipitsa, nasunga dzanja lace osacita nalo coipa ciri conse.

3. Mlendo amene wadziphatika yekha kwa Yehova asanene, kuti, Yehova adzandilekanitsa ndithu ndi anthu ace; pena mfule asanene, Taonani ine ndiri mtengo wouma.

4. Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa Ine, nigwira zolimba cipangano canga,

5. Kwa iyo ndidzapatsa m'nyumba yanga ndi m'kati mwa makoma anga malo, ndi dzina loposa la ana amuna ndi akazi; ndidzawapatsa dzina lacikhalire limene silidzadulidwa.

6. Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ace, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba cipangano canga;

7. naonso ndidzanka nao ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa pa guwa la nsembe langa; pakuti nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.

8. Ambuye Yehova amene asonkhanitsa otayika a Israyeli ati, Komabe ndidzasonkhanitsa ena kwa iye, pamodzi ndi osonkhanitsidwa ace ace.

9. Inu zirombo zonse za m'thengo, idzani kulusa, inde zirombo inu nonse za m'nkhalango.

10. Alonda ace ali akhungu, iwo onse ali opanda nzeru; iwo onse ali agaru acete, osatha kuuwa; kungolota, kugona pansi, kukonda kugona tulo.

11. Inde agaru ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira ku njira zao, yense kutsata phindu lace m'dera lace.

12. Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta cakumwa caukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikuru loposa ndithu.