Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48
  49. 49
  50. 50
  51. 51
  52. 52
  53. 53
  54. 54
  55. 55
  56. 56
  57. 57
  58. 58
  59. 59
  60. 60
  61. 61
  62. 62
  63. 63
  64. 64
  65. 65
  66. 66

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Aneneratu za Etiopia

1. Ha, dziko lakukupuza mapiko, liri tsidya lija la nyanja za Etiopia;

2. limene litumiza mithenga panyanja m'ngalawa zatnabungwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msanga msanga ku mtundu wa anthu atari ndi osalala, kwa mtundu woopsya cikhalire cao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lace nyanja ziligawa!

3. Inunonseakukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika pa dziko lapansi, potukulidwa cizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.

4. Pakuti Yehova watero kwa ine, Ine ndidzakhala cete, ndipo ndidzayang'ana mokhala cete, ndipo ndidzayang'ana mokhalamo Ine, monga kuwala kotentha kwa dzuwa, monga mtambo wa mame m'kutentha kwa masika.

5. Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kucha, iye adzadzombolera tinthambi ndi mphopo, ndi nthambi zotasa adzazicotsa ndi kuzisadza.

6. Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zirombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zirombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.

7. Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu atari ndi osalala, yocokera kwa mtundu woopsya cikhalire cao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lace nyanja ziligawa, ku malo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.