Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31
  32. 32
  33. 33
  34. 34
  35. 35
  36. 36
  37. 37
  38. 38
  39. 39
  40. 40
  41. 41
  42. 42
  43. 43
  44. 44
  45. 45
  46. 46
  47. 47
  48. 48
  49. 49
  50. 50
  51. 51
  52. 52
  53. 53
  54. 54
  55. 55
  56. 56
  57. 57
  58. 58
  59. 59
  60. 60
  61. 61
  62. 62
  63. 63
  64. 64
  65. 65
  66. 66

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Aneneratu za kuonongeka kwa Moabu

1. Katundu wa Moabu.Pakuti usiku umodzi Ara wa ku Moabu wapasuka, nakhala cabe; usiku umodzi Kiri wa Moabu wapasuka, nakhala cabe.

2. Akwera kukacisi, ndi ku Dibo, kumisanje, kukalira; pa Nebo ndi pa Medeba a Moabu pali kulira; pamitu pao ponse pali dazi, ndebvu zonse zametedwa.

3. M'makwalala mwao adzimangira ciguduli m'cuuno, pamwamba pa nyumba zao, ndi m'malo a mabwalo ao, yense akuwa, naliritsa kwambiri.

4. Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m'kati mwace.

5. Mtima wanga upfuula cifukwa ca Moabu: akuru ace athawira ku Zoari, ku Eglatiselisiya; pakuti pa cikweza ca Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horanaimu akweza mpfuu wa cionongeko.

6. Pakuti pa madzi a Nimirimi padzakhala mabwinja; papeza udzu wafota, msipu watha.

7. Cifukwa cace zocuruka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo ku mtsinje wa mabango.

8. Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Moabu; kukuwa kwace kwafikira ku Eglaimu, ndi kukuwa kwace kwafikira ku Beerelimu.

9. Pakuti madzi a Dimoni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa! Dimoni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Moabu, ndi pa otsala am'dziko.