Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 22:9-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.

10. Ndipo pamene anafikira mbali ya ku Yordano, ndilo la m'dziko la Kanani, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga ku Yordano guwa la nsembe, guwa lalikuru maonekedwe ace.

11. Ndipo ana a Israyeli anamva anthu akuti, Taonani ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anamanga guwa la nsembe pandunji pa dziko la Kanani, ku mbali ya ku Yordano, ku mbali ya ana a Israyeli.

12. Pamene ana a Israyeli anamva ici msonkhano wonse wa ana a Israyeli anasonkhana ku Silo, kuti awakwerere kuwathira nkhondo.

13. Ndipo ana a Israyeli anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, Pinehasi mwana wa Eleazare wansembe,

14. ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mapfuko onse a Israyeli; yense wa iwowa ndiye mkuru wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israyeli.

15. M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ku dziko la Gileadi, ananena nao ndi kuti,

16. Utero msonkhano wonse wa Yehova, Colakwa ici nciani mwalakwira naco Mulungu wa Israyeli, ndi kumtembenukira Yehova lero line kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?

17. Kodi mphulupulu ya ku Peori iticepera, imene sitinadziyeretsera mpaka lero lino, ungakhale mliri unadzera msonkhano wa Yehova,

18. kuti mubwerera lero line kusatsata Yehova? ndipo kudzakhala kuti popeza lero mupikisana ndi Yehova, mawa adzakwiyira msonkhano wonse wa Israyeli.

19. Koma mukayesa dziko La colowa canu ncodetsa, olokani kulowa m'dziko lacolowaca Yehova m'mene cihemaca Yehovacikhalamo, nimukhale naco colowa pakati pa ife; koma musapikisana ndi Yehova kapena kupikisana nafe, ndi kudzimangira nokha guwa la nsembe, pamodzi ndi guwa la nsembe la Yehova Mulungu wathu.

20. Kodi Akani mwana wa Zera sanalakwa m'coperekedwaco, ndipo mkwiyo unagwera msonkhano wonse wa Israyeli? osangoonongeka yekha munthuyo mu mphulupulu yace.

21. Pamenepo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anayankha, nanena ndi akuru a mabanja a Israyeli,

22. Yehova Cauta Mulungu, Yehova Cauta Mulungu, iye adziwa, ndi Israyeli adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,

23. tadzimangira guwa la nsembe, kubwerera kusamtsata Yehova, musatipulumutsa lero lino; kapena ngati kufukizapo nsembe yopsereza, kapena nsembe yaufa, kapena kuperekapo nsembe zoyamika, acifunse Yehova mwini wace;

24. ndipo ngati ife sitinacita ici cifukwa ca kuopa mlandu, ndi kuti, Masiku akudzawo ana anu akadzanena ndi ana athu, ndi kuti, Muli ciani inu kwa Yehova Mulungu wa Israyeli?

25. pakuti Yehova anaika Yordano ukhale malire pakati pa ife ndi inu, ana a Rubeni, ndi ana a Gadi; mulibe gawo ndi Yehova; motero ana anu adzaleketsa ana athu asaope. Yehova.

26. Cifukwa cace tinati, Tiyeni tikonzeretu zotimangira guwa la nsembe, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai;

27. koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu; ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikacita nchito ya Yehova pamaso pace ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.

28. Cifukwa cace tinati, Kudzali, akadzatero kwa ife, kapena kwa mibadwo yathu m'tsogolomo, kuti tidzati, Tapenyani, citsanzo ca guwa la nsembe la Yehova, comanga makolo athu, si kufukizapo nsembe yopsereza ai, kapena nsembe yophera ai, koma ndilo mboni pakati pa ife ndi inu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 22