Utero msonkhano wonse wa Yehova, Colakwa ici nciani mwalakwira naco Mulungu wa Israyeli, ndi kumtembenukira Yehova lero line kusamtsatanso, popeza munadzimangira guwa la nsembe kupikisana ndi Yehova lero lino?