nanena nao ndi kuti, Bwererani naco cuma cambiri ku mahema anu, ndi zoweta zambirimbiri, ndi siliva, ndi golidi, ndi mkuwa, ndi citsulo, ndi maraya ambirimbiri; mugawane nao abale anu zofunkha kwa adani anu.