Ndipo ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati anabwerera, nacoka kwa ana a Israyeli ku Silo, ndiwo wa m'dziko la Kanani kumka ku dziko la Gileadi, ku dziko lao lao, limene anakhala eni ace, monga mwa lamulo la Yehova, mwa dzanja la Mose.