Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 44:9-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.

10. Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?

11. Taonani anzace onse adzakhala ndi manyazi, ndi amisiri ace ndi anthu; asonkhane onse pamodzi, aimirire; adzaopa, iwo onse adzakhala ndi manyazi.

12. Wacipala acita zace ndi nsompho, nagwira nchito ndi makala, nafanizira fanolo ndi nyundo, nagwira nchito yace ndi mkono wace wamphamvu; inde, ali ndi njala, ndipo mphamvu zace zilephera; iye samwa madzi, nalefuka.

13. Mmisiri wa mitengo atambalitsa cingwe; nalilemba ndi colembera, nalikonza ndi ncerero, nalilemba ndi zolinganizira, nalifanizira monga maonekedwe a munthu, monga munthu wokongola, kuti likhale m'nyumba.

14. Iye adzidulira yekha mikungudza, natenga mtengo wambawa, ndi wathundu, ndi kudzisankhira yekha wina wa mitengo ya nkhalango; naoka mtengo wamlombwa, mvula niukulitsa.

15. Ndipo udzakhala kuti munthu autenthe; iye natengako, nauotha moto; inde auyatsa, naoca mkate; inde, apanga mlungu, naulambira, naupanga fano losema, naligwadira.

16. Iye atenthako mbali yina pamoto; ndi mbali yinayo adya nyama; akazinga zokazinga, nakhuta, inde, aotha moto, nati, Ha, ndakongonoka, ndauona moto.

17. Ndipo cotsalaco apanga mlungu, ngakhale fano lace losema; iye aligwadira, nalipembedza, nalipemphera nati, Ndipulumutse ine, cifukwa kuti ndinu mulungu wanga.

18. Iwo sadziwa, kapena kuzindikira, cifukwa pamaso pao papakidwa thope, kuti sangaone, ndi m'mitima mwao kuti sangadziwitse.

19. Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali yina pamoto, inde ndaocanso mkate pamakala pace, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndicipange cotsala cace, cikhale conyansa? ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo?

20. Iye adya phulusa; mtima wodzinyenga wampambutsa, kuti iye sangapulumutse moyo wace, pena kunena, Kodi simuli kunama m'dzanja langa lamanja?

21. Kumbukira zinthu izi, Yakobo; ndi Israyeli, pakuti iwe ndiwe mtumiki wanga; ndakuumba, iwe ndiwe mtumiki wanga, Israyeli, sindidzakuiwala.

22. Ine ndafafaniza monga mtambo wocindikira zolakwa zako, ndi monga mtambo macimo ako; bwerera kwa Ine, pakuti ndakuombola.

23. Yimbani m'mwamba inu, pakuti Yehova wacicita ico; kuwani inu, mbali za pansi pa dziko; yimbani mapiri inu; nkhalango iwe, ndi mitengo yonse m'menemo; cifukwa kuti Yehova wapulumutsa Yakobo, ndipo adzadzilemekezetsa yekha mwa Israyeli.

24. Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lopansi; ndani ali ndi Ine?

25. Ndine amene nditsutsa zizindikilo za matukutuku, ndi kucititsa misala oombeza ula; ndi kubwezera m'mbuyo anthu anzeru, ndi kupusitsa nzeru zao:

Werengani mutu wathunthu Yesaya 44