Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 4:9-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Belitsazara iwe, mkuru wa alembi, popeza ndidziwa kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera, ndi kuti palibe cinsinsi cikusautsa, undifotokozere masomphenya a loto langa ndalotali, ndi kumasulira kwace.

10. Masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga ndi awa: Ndinapenya ndi kuona mtengo pakati pa dziko lapansi, msinkhu wace ndi waukuru.

11. Mtengowo unakula, nulimba, ndi msinkhu wace unafikira kumwamba, nuonekera mpaka cilekezero ca dziko lonse lapansi.

12. Masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zinacuruka, ndi m'menemo munali zakudya zofikira onse, nyama za kuthengo zinatsata mthunzi wace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinafatsa m'thambi zace, ndi nyama zonse zinadyako.

13. Ndinaona m'masomphenya a m'mtima mwanga pakama panga, taonani, mthenga woyera anatsika kumwamba.

14. Anapfuulitsa, natero, Likhani mtengowo, sadzani nthambi zace, yoyolani masamba ace, mwazani zipatso zace, nyama zicoke pansi pace, ndi mbalame pa nthambi zace.

15. Koma siyani citsa ndi mizu yace m'nthaka, comangidwa ndi mkombero wa citsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo; ncokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lace likhale pamodzi ndi nyama ziri m'macire a m'dziko.

16. Mtima wace usandulike, usakhalenso mtima wa munthu, apatsidwe mtima wonga wa nyama, nizimpitire nthawi zisanu ndi ziwiri.

17. Citsutso ici adacilamulira amithenga oyerawo, anacifunsa, nacinena, kuti amoyo adziwe kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira wolubukira anthu.

18. Loto ili ndinaliona ine mfumu Nebukadinezara; ndipo iwe, Belitsazara, undifotokozere kumasulira kwace, popeza anzeru onse a m'ufumu wanga sakhoza kundidziwitsa kumasulira kwace; koma iwe ukhoza, popeza mwa iwe muli mzimu wa milungu yoyera.

19. Pamenepo Danieli, dzina lace ndiye Belitsazara anadabwa nthawi, namsautsa maganizo ace. Mfumu inayankha, niti, Belitsazara, lisakusautse lotoli, kapena kumasulira kwace. Belitsazara anayankha, nati, Mbuye wanga, lotoli likadakhala la iwo akudana nanu, ndi kumasulira kwace kwa iwo akuutsana nanu.

20. Mtengo mudauona umene unakula, nukhala wolimba, nufikira kumwamba msinkhu wace, nuonekera pa dziko lonse lapansi,

21. umene masamba ace anali okoma, ndi zipatso zace zocuruka, ndi m'menemo munali cakudya cofikira onse, umene nyama za kuthengo zinakhala pansi pace, ndi mbalame za m'mlengalenga zinapeza pokhala pao pa nthambi yace;

22. ndinu, mfumu; mwakula, mwalimba, pakuti ukulu wanu wakula, nufikira kumwamba, ndi ufumu wanu ku cilekezero ca dziko lapansi.

23. Tsono, kuti mfumu inaona mthenga woyera wotsika kumwamba, ndi kuti, Likhani mtengowo ndi kuuononga, koma siyani citsa cace ndi mizu m'nthaka, comangidwa ndi mkombero wa citsulo ndi mkuwa, mu msipu wa kuthengo, nicikhale cokhathamira ndi mame a kumwamba, ndi gawo lace likhale pamodzi ndi nyama za kuthengo, mpaka zitampitira nthawi zisanu ndi ziwiri;

24. kumasulira kwace ndi uku, mfumu; ndipo cilamuliro ca Wam'mwambamwamba cadzera mbuye wanga mfumu:

25. kuti adzakuingitsani kukucotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama za kuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, nizidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira m'ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna mwini.

26. Ndipo kuti anauza asiye citsa ndi mizu ya mtengo, ufumu wanu udzakhazikikira inu, mukakatha kudziwa kuti Kumwamba kumalamulira.

Werengani mutu wathunthu Danieli 4