Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 28:8-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Sauli anadzizimbaitsa nabvala zobvala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire ali yense ndidzakuchulira dzina lace.

9. Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa cimene anacita Sauli, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; cifukwa ninji tsono mulikuchera moyo wanga msampha, kundifetsa.

10. Ndipo Sauli anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe cilango cidzakugwera cifukwa ca cinthu ici.

11. Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samueli.

12. Ndipo mkaziyo pakuona Samueli, anapfuula ndi mau akuru; ndi mkaziyo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli.

13. Ndipo mfumuvo inanena naye, Usaope, kodi ulikuona ciani? Mkaziyo nanena ndi Sauli, Ndirikuona milungu irikukwera kuturuka m'kati mwa dziko.

14. Ndipo ananena naye, Makhalidwe ace ndi otani? nati iye, Nkhalamba irikukwera yobvala mwinjiro. Pamenepo Sauli anazindikira kuti ndi Samueli, naweramitsa nkhope yace pansi, namgwadira.

15. Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Wandibvutiranji kundikweretsa kuno? Sauli nayankha, Ndirikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandicokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; cifukwa cace ndakuitanani, kuti mundidziwitse cimene ndiyenera kucita.

16. Ndip'o Samueli ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakucokera, nasandulika mdani wako?

17. Ndipo Yehova yekha wacita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuucotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.

18. Cifukwa sunamvera mau a Yehova, ndi kukwaniritsa mkwiyo wace woopsa pa Ameleki, cifukwa cace Yehova wakucitira cinthu ici lero.

19. Ndiponso Yehova adzapereka Israyeli pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisrayeli m'dzanja la Afilisti.

20. Pomwepo Sauli anagwa pansi tantha, naopa kwakukuru, cifukwa ca mau a Samueli; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wace wonse anakhala osadya kanthu.

21. Ndipo mkaziyo anafika kwa Sauli, naona kuti ali wobvutika kwambiri, nanena naye, Onani, mdzakazi wanu anamvera mau anu, ndipo ndinataya moyo wanga, ndi kumvera mau anu munalankhula ndi ine.

22. Cifukwa cace tsono, mumverenso mau a mdzakazi wanu, nimundilole kuika kakudya pamaso panu; ndipo mudye, kuti mukhale ndi mphamvu pakumuka.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 28