Tsono Sauli anati kwa anyamata ace, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ace anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.