Pomwepo Sauli anagwa pansi tantha, naopa kwakukuru, cifukwa ca mau a Samueli; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wace wonse anakhala osadya kanthu.