Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27
  28. 28
  29. 29
  30. 30
  31. 31

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Madyerero a Nzeru

1. Nzeru yamanga nyumba yace,Yasema zoimiritsa zace zisanu ndi ziwiri;

2. Yaphera nyama yace, nisanganiza vinyo wace,Nilongosolanso pa gome lace.

3. Yatuma anamwali ace, iitanaPa misanje ya m'mudzi.

4. Wacibwana yense apambukire kuno;Iti kwa yense wosowa nzeru,

5. Tiyeni, idyani cakudya canga;Nimumwe vinyo wanga ndamsanganiza.

6. Lekani, acibwana inu, nimukhale ndi moyo;Nimuyende m'njira ya nzeru.

7. Woweruza munthu wonyoza adzicititsa yekha manyazi;Yemwe adzudzula wocimwa angodetsa mbiri yace yace.

8. Usadzudzule wonyoza kuti angakude;Dzudzula wanzeru adzakukonda.

9. Ukacenjeza wanzeru adzakulitsa nzeru yace;Ukaphunzitsa wolungama adzaonjezera kuphunzira,

10. Ciyambi ca nzeru ndico kuopa Yehova;Kudziwa Woyerayo ndiko luntha;

11. Pakuti mwa ine masiku ako adzacuruka,Zaka za moyo wako zidzaonjezedwa.

12. Ukakhala wanzeru, si yako yako nzeruyo?Ndipo ukanyoza udzasauka wekha.

13. Utsiru umalongolola,Ngwa cibwana osadziwa kanthu.

14. Ukhala pa khomo la nyumba yace,Pampando pa misanje ya m'mudzi

15. Kuti uitane akupita panjira,Amene angonkabe m'kuyenda kwao,

16. Wacibwana ndani? Apambukire kuno.Ati kwa yense wopanda nzeru,

17. Madzi akuba atsekemera,Ndi cakudya cobisika cikoma.

18. Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko;Omwe acezetsa utsiru ali m'manda akuya.