Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 28:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali masiku aja, Afilisti anasonkhanitsa pamodzi makamu ao onse kunkhondo, kuti akaponyane ndi Aisrayeli. Ndipo Akisi ananena ndi Davide, Dziwa kuti zoonadi, udzaturuka nane ndi nkhondo, iwe ndi anthu ako.

2. Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe cimene mnyamata wanu adzacita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Cifukwa cace ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.

3. M'menemo Samueli ndipo atafa, ndipo Aisrayeli onse atalira maliro ace, namuika m'Rama, m'mudzi mwao. Ndipo Sauli anacotsa m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula onse.

4. Ndipo Afilisti anasonkhana, nadza namanga misasa ku Sunemu; ndipo Sauli anasonkhanitsa Aisrayeli onse, namanga iwo ku Giliboa.

5. Ndipo pamene Sauli anaona khamu la Afilisti, anaopa, ndi mtima wace unanjenjemera kwakukuru.

6. Ndipo pamene Sauli anafunsira kwa Yehova, Yehova sanamyankha ngakhale ndi maloto, kapena ndi Urimu, kapena ndi aneneri.

7. Tsono Sauli anati kwa anyamata ace, Mundifunire mkazi wobwebweta, kuti ndimuke kwa iye ndi kumfunsira. Ndipo anyamata ace anati kwa iye, Onani ku Endori kuli mkazi wobwebweta.

8. Ndipo Sauli anadzizimbaitsa nabvala zobvala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire ali yense ndidzakuchulira dzina lace.

9. Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa cimene anacita Sauli, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; cifukwa ninji tsono mulikuchera moyo wanga msampha, kundifetsa.

10. Ndipo Sauli anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe cilango cidzakugwera cifukwa ca cinthu ici.

11. Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samueli.

12. Ndipo mkaziyo pakuona Samueli, anapfuula ndi mau akuru; ndi mkaziyo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli.

13. Ndipo mfumuvo inanena naye, Usaope, kodi ulikuona ciani? Mkaziyo nanena ndi Sauli, Ndirikuona milungu irikukwera kuturuka m'kati mwa dziko.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 28