Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Samueli 17:36-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

36. Ine kapolo wanu ndinapha mkango ndi cimbalangondo zonse ziwiri; ndipo Mfilisti uyu wosadulidwa adzakhala ngati mmodzi wa izo, popeza wanyoza makamu a Mulungu wamoyo.

37. Nati Davide, Yehova wakundipulumutsa pa mphamvu ya mkango, ndi mphamvu ya cimbalangondo, Iyeyu adzandipulumutsa m'dzanja la Mfilisti uyu, Ndipo Sauli anati kwa Davide, Muka, Yehova akhale nawe.

38. Ndipo Sauli anabveka Davide zobvala zace za iye yekha, nambveka cisoti camkuwa pamutu pace, nambvekanso maraya aunyolo.

39. Ndipo Davide anamanga lupanga lace pamwamba pa zobvala zace, nayesa kuyenda nazo; popeza sanaziyesera kale. Ndipo Davide anati kwa Sauli, Sindikhoza kuyenda ndi izi; pakuti sindinazizolowera. Nazibvula Davide.

40. Natenga ndodo yace m'dzanja lace nadzisankhira miyala isanu yosalala ya mumtsinje, naiika m'thumba la kubusa, limene anali nalo ndilo cibete; ndi coponyera miyala cinali m'dzanja lace, momwemo anayandikira kwa Mfilistiyo.

41. Ndipo Mfilistiyo anadza, nayandikira kwa Davide; ndi wonyamula cikopa cace anamtsogolera.

42. Ndipo Mfilisti pakumwazamwaza maso, ndi kuona Davide, anampeputsa; popeza anali mnyamata cabe, wofiirira, ndi wa nkhope yokongola.

43. Ndipo Mfilisti anati kwa Davide, Ine ndine garu kodi, kuti iwe ukudza kwa ine ndi ndodo? Ndi Mfilistiyo anatukwana Davide nachula milungu yace.

44. Ndipo Mfilistiyo anati kwa Davide, Idza kuno kwa ine, ndidzapatsa mnofu wako kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za kuthengo.

45. Ndipo Davide anati kwa Mfilistiyo, Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, ndi mkondo, ndi nthungo; koma ine ndafika kwa iwe m'dzina la Yehova wa makamu, Mulungu wa ankhondo a Israyeli amene iwe unawanyoza.

46. Lero lino Yehova adzakupereka iwe m'dzanja langa, ndipo ndidzakukantha, ndi kukucotsera mutu wako. Ndipo lero ndidzapatsa mitembo ya makamu a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo za dziko lapansi; kuti dziko lonse likazindikire kuti kwa Israyeli kuli Mulungu.

47. Ndi msonkhano wonse uno udzazindikira kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga, kapena ndi mkondo; pakuti Yehova ndiye mwini nkhondo, ndipo iye adzakuperekani inu m'manja athu.

48. Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.

49. Ndipo Davide anapisa dzanja lace m'thumba mwace, naturutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi cafufumimba.

50. Comweco Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa coponyera cace, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.

51. Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lace, nalisolola m'cimace, namtsiriza nadula nalo mutu wace. Ndipo pakuona Afilisti kuti ciwinda cao cidafa, anathawa.

52. Ndipo anthu a Israyeli ndi Ayuda ananyamuka, napfuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kucigwako, ndi ku zipata za Ekroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saraimu, kufikira ku Gad ndi ku Ekroni.

53. Ndipo ana a Israyeli atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.

Werengani mutu wathunthu 1 Samueli 17