Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Mafumu 11:15-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Pakuti pamene Davide adali m'Edomu, ndipo Yoabu kazembe wa nkhondo adanka kukaika akufawo, atapha amuna onse m'Edomu;

16. pakuti Yoabu ndi Aisrayeli onse anakhalako miyezi isanu ndi umodzi, mpaka atawapha amuna onse m'Edomu;

17. Hadadi uja anathawa, iyeyo ndi a ku Edomu ena, akapolo a atate wace pamodzi naye, kumka ku Aigupto, Hadadiyo akali mwana.

18. Ndipo anacoka ku Midyani nafika ku Parani, natenga anthu a ku Parani pamodzi nao, nafika ku Aigupto kwa Farao mfumu ya Aigupto, ameneyo anampatsa nyumba, namnenera zakudya, nampatsako dziko.

19. Ndipo Farao anamkomera mtima ndithu Hadadiyo, nampatsa mkazi ndiye mbale wa mkazi wace, mbale wace wa Takipenesi mkazi wamkulu wa mfumu.

20. Ndipo mbale wa Takipenesi anamuonera Genubati mwana wace, ameneyo Takipenesi anamletsera kuyamwa m'nyumba ya Farao, ndipo Genubati anakhala m'banja la Farao pamodzi ndi ana amuna a Farao.

21. Ndipo atamva Hadadi ku Aigupto kuti Davide anagona ndi makolo ace, ndi kuti Yoabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.

22. Tsono Farao anati kwa iye, Koma cikusowa iwe nciani kwa ine, kuti ufuna kumuka ku dziko la kwanu? Nayankha iye, Palibe kanthu, koma mundilole ndimuke ndithu.

23. Ndipo Mulungu anamuutsira mdani wina, ndiye Rezoni mwana wa Eliyada, amene adathawa mbuye wace Hadadezeri mfumu ya ku Zoba.

24. Iye nasonkhanitsa anthu, nakhala kazembe wa nkhondo, muja Davide anawapha a ku Zobawo, napita ku Damasiko, hakhala komweko, nakhala mfumu ya ku Damasiko.

25. Ndipo iye anali mdani wa Israyeli masiku onse a Solomo, kuonjezerapo coipa anacicita Hadadi, naipidwa nao Aisrayeli, nakhala mfumu ya ku Aramu.

26. Ndipo Yerobiamu mwana wa Nebati M-efrati wa ku Zereda mnyamata wa Solomo, dzina la amace ndiye Zeruwa, mkazi wamasiye, iyenso anakweza dzanja lace pa mfumu.

27. Ndipo cifukwa cakukweza iye dzanja lace pa mfumu ndi cimeneci: Solomo anamanga Milo, namanganso pogumuka pa linga la mudzi wa Davide atate wace.

28. Ndipo munthu ameneyo Yerobiamu anali ngwazi; ndipo pamene Solomo anamuona mnyamatayo kuti ngwacangu, anamuika akhale woyang'anira wa nchito yonse ya nyumba ya Yosefe.

29. Ndipo kunali nthawi yomweyo kuti Yerobiamu anaturuka m'Yerusalemu, ndipo mneneri Ahiya wa ku Silo anampeza m'njira; tsono iyeyo anabvaliratu cobvala catsopano, ndipo iwo awiri anali okha kuthengo.

30. Ndipo Ahiyayo anagwira cobvala cace catsopano, nacing'amba khumi ndi pawiri.

Werengani mutu wathunthu 1 Mafumu 11