Ndipo atamva Hadadi ku Aigupto kuti Davide anagona ndi makolo ace, ndi kuti Yoabu kazembe wa nkhondo adafanso, Hadadi ananena ndi Farao, Mundilole ndimuke ku dziko la kwathu.