naonso ndidzanka nao ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m'nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zao zopsereza ndi nsembe zao zidzalandiridwa pa guwa la nsembe langa; pakuti nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.