Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 52:13-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za m'Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikuru zonse, anazitentha ndi moto.

14. Ndipo nkhondo yonse ya Akasidi, imene inali ndi kapitao wa alonda, inagumula makoma onse a Yerusalemu pomzungulira pace.

15. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende anthu aumphawi, ndi anthu otsala amene anatsala m'mudzi, ndi amene anapandukira, kutsata mfumu ya ku Babulo, ndi otsala a unyinjiwo.

16. Koma Nebuzaradani kapitao wa alonda anasiya aumphawi a padziko akhale akulima mphesa ndi akulima m'minda.

17. Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazityolatyola, nanka nao mkuwa wace wonse ku Babulo.

18. Ndiponso miphika, ndi zoolera, ndi mbano zao, ndi mbale, ndi zipande, ndi zipangizo zonse zamkuwa zimene anatumikira nazo, anazicotsa.

19. Ndi zikho, ndi zopalira moto, ndi mbale, ndi miphika, ndi zoikapo nyali, ndi zipande, ndi mitsuko; ndi golidi, wa zija zagolidi, ndi siliva, wa zija zasiliva, kapitao wa alonda anazicotsa.

20. Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomo anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanatha kuyesa kulemera kwace.

21. Koma nsanamirazo, utari wace wa nsanamira yina unafikira mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndi cingwe ca mikono khumi ndi iwiri cinaizinga; kucindikira kwace kunali zala zinai; inali yagweregwere.

22. Ndipo korona wamkuwa anali pamwamba pace; utari wace wa korona mmodzi unali wa mikono isanu, ndi made ndi makangaza pakorona pozungulira pace, onse amkuwa: nsanamira inzace yomwe inali nazo zonga zomwezi, ndi makangaza.

23. Ndipo pambali pace panali makangaza makumi asanu ndi anai kudza asanu ndi limodzi; ndipo makangaza onse anali zana limodzi pamade pozungulira pace.

24. Ndipo kapitao wa alonda anatenga Seraya mkuru wansembe, ndi Zefaniya wansembe waciwiri, ndi akudikira pakhomo atatu;

25. ndipo m'mudzi anatenga kazembe amene anali woyang'anira anthu a nkhondo ndi amuna asanu ndi awiri a iwo akuona nkhope ya mfumu, amene anapezedwa m'mudzi; ndi mlembi wa kazembe wa nkhondo, amene akamemeza anthu a m'dziko; ndi amuna makumi asanu ndi limodzi a anthu a m'dziko, amene anapezedwa pakati pa mudzi.

26. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga iwo, nadza nao kwa mfumu ya ku Babulo ku Ribila.

27. Ndipo mfumu ya ku Babulo anawakantha, nawapha pa Ribila m'dziko la Hamati. Comweco Yuda anatengedwa ndende kuturuka m'dziko lace.

28. Amenewa ndi anthu amene Nebukadirezara anatenga ndende: caka cacisanu ndi ciwiri, Ayuda zikwi zitatu kudza makumi awiri ndi atatu;

29. caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara iye anatenga ndende kucokera m'Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;

30. caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Nebukadirezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

31. Ndipo panali caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babulo anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namturutsa iye m'ndende;

32. nanena naye bwino, naika mpando wace upose mipando ya mafumu amene anali naye m'Babulo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 52