Nsanamira ziwirizo, thawale limodzilo, ndi ng'ombe zamkuwa zinali pansi pa zoikapo, zimene mfumu Solomo anazipangira nyumba ya Yehova; mkuwa wa zipangizo zonsezi sanatha kuyesa kulemera kwace.