Ndi mizati yamkuwa imene inali m'nyumba ya Yehova, ndi zoikapo ndi thawale lamkuwa zimene zinali m'nyumba ya Yehova, Akasidi anazityolatyola, nanka nao mkuwa wace wonse ku Babulo.