Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Nehemiya 9:8-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndipo munampeza mtima wace wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zace; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.

9. Ndipo munapenya msauko wa makolo athu m'Aigupto, nimunamva kupfuula kwao ku Nyanja Yofiira,

10. nimunacitira zizindikilo ndi zodabwiza Farao ndi akapolo ace onse, ndi anthu onse a m'dziko lace; popeza munadziwa kuti anawacitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.

11. Ndipo munagawanitsa nyanja pamaso pao, napita iwo pakati pa nyanja pouma, ndipo munaponya mozama owalondola, ngati mwala m'madzi olimba.

12. Munawatsogoleranso usana ndi mtambo woti njo, ndi moto tolo usiku, kuwaunikira m'njira akayendamo.

13. Munatsikiranso pa phiri la Sinai, nimunalankhula nao mocokera m'Mwamba, ndipo munawapatsa maweruzo oyenera, ndi cilamulo coona, malemba, ndi malamulo okoma;

14. ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi cilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;

15. ndi mkate wocokera m'mwamba munawapatsa pa njala yao; ndi madzi oturuka m'thanthwe munawaturutsira pa ludzu lao, ndi kuwauza alowe, nalandire dziko limene mudakwezapo dzanja lanu kuwapatsa.

16. Koma iwo ndi makolo athu anacita modzikuza, naumitsa khosi lao, osamvera malamulo anu,

17. nakana kumvera, osakumbukilansozodabwiza zanu munazicita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kumka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wacisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wocuruka cifundo; ndipo simunawasiya.

18. Ngakhale apa atadzipangira mwana wa ng'ombe woyenga, nati, Suyu Mulungu wako anakukweza kucokera ku Aigupto, nacita zopeputsa zazikuru;

19. koma Inu mwa nsoni zanu zazikuru simunawasiya m'cipululu; mtambo woti njo sunawacokera usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.

20. Munawapatsanso mzimu wanu wokoma kuwalangiza, ndipo simunawamana mana anu pakamwa pao; munawapatsanso madzi pa ludzu lao.

21. Ndipo munawalera zaka makumi anai m'cipululu, osasowa kanthu iwo; zobvala zao sizinatha, ndi mapazi ao sanatupa.

22. Munawapatsanso maufumu, ndi mitundu ya anthu, nimunawagawa m'madera, motero analandira likhale lao lao dziko la Sihoni, ndilo dziko la mfumu ya ku Hesiboni, ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basana.

23. Ana aonso munawacurukitsa monga nyenyezi za m'mwamba, nimunawalowetsa m'dziko mudalinena kwa makolo ao, alowemo likhale lao lao.

24. Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale lao lao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti acite nao cifuniro cao.

Werengani mutu wathunthu Nehemiya 9