ndipo munampeza mtima wace wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zace; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.