Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Popereka nsembe

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Nena ndi Aroni, ndi ana ace amuna, ndi ana a Israyeli onse, nuti nao, Ici ndi cimene Yehova wauza, ndi kuti,

3. Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli akapha ng'ombe, kapena mwana wa nkhosa, kapena mbuzi, m'cigono, kapena akaipha kunja kwa cigono,

4. osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuti aipereke copereka ca Yehova, ku bwalo la kacisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wocimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumcotsa pakati pa anthu a mtundu wace;

5. kotero kuti ana a Israyeli azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.

6. Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo pa guwa la nsembe la Yehova, pa khomo la cihema cokomanako, natenthe mafuta akhale pfungo lokoma lokwera kwa Yehova.

7. Ndipo asamapheranso ziwanda nsembe zao, zimene azitsata ndi cigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.

8. Ndipo uzinena nao, Munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,

9. osadza nayo ku khomo la cihema cokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

Aletsedwa kudya mwazi

10. Ndipo munthu ali yense wa mbumba ya Israyeli, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uli wonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumcotsa kwa anthu a mtundu wace.

11. Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, ucite cotetezera moyo wanu; pakuti wocita cotetezera ndiwo mwazi, cifukwa ca moyo wace.

12. Cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo ali yense wakugoneramwa inu asamadya mwazi.

13. Ndipo munthu ali yense wa ana a Israyeli, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wace naufotsere ndi dothi.

14. Pakuti ndiwo moyo wa: nyama zonse, mwazi wace ndiwo moyo wace; cifukwa cace ndinanena kwa ana a Israyeli, Musamadya mwazi wa nyama iri yonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wace; ali yense akaudya adzasadzidwa.

15. Ndipo ali yense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m'dziko kapena mlendo, azitsuka nsaru zace, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.

16. Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lace, adzasenza mpholupulu yace.