Mitu

  1. 1
  2. 2
  3. 3
  4. 4
  5. 5
  6. 6
  7. 7
  8. 8
  9. 9
  10. 10
  11. 11
  12. 12
  13. 13
  14. 14
  15. 15
  16. 16
  17. 17
  18. 18
  19. 19
  20. 20
  21. 21
  22. 22
  23. 23
  24. 24
  25. 25
  26. 26
  27. 27

Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

Za kuyeretsedwa kwa mkazi

1. Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2. Nena ndi ana a Israyeli, ndi kuti, Akaima mkazi, nakabala mwana wamwamuna, adzakhala wodetsedwa masiku asanu ndi awiri; monga masiku ace akukhala padera, podwala iye, adzakhalawodetsedwa.

3. Ndipo tsiku lacisanu ndi citatu adule khungu la mwanayo.

4. Ndipo akhale m'mwazi wa kumyeretsa kwace masiku makumi atatu kudza atatu; asakhudze kanthu kopatulika, kapena kulowa m'malo opatulika, kufikira adakwanira masiku a kumyeretsa kwace.

5. Koma akabala mwana wamkazi, akhale wodetsedwa masabata awiri, monga umo amakhala padera; ndipo adzakhala m'mwazi wa kumyeretsa kwace masiku makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi.

6. Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwace pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwana wa nkhosa wa caka cimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yaucimo, ku khomo la cihema cokomanako, kwa wansembe;

7. ndipo iye abwere nayo pamaso pa Yehova, namcitire comtetezera mkaziyo, ndipo adzakhala woyeretsedwa wocira kukha mwazi kwace.

8. Ici ndi cilamulo ca kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo cuma cace cikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yaucimo; ndi wansembe amcitire comtetezera, ndipo adzakhalawoyera.