Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Levitiko 16:16-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. nacitire cotetezera malo opatulika, cifukwa ca kudetsedwa kwa ana a Israyeli, ndi cifukwa ca zolakwa zao, monga mwa zocimwa zao zonse; nacitire cihema cokomanako momwemo, cakukhala nao pakati pa zodetsa zao.

17. Ndipo musakhale munthu m'cihema cokomanako pakulowa iye kucita cotetezera m'malo opatulika, kufikira aturuka, atacita cotetezera yekha, ndi mbumba yace, ndi msonkhano wonse wa Israyeli.

18. Ndipo aturukire guwa la nsembe lokhala pamaso pa Yehova ndi kulicitira cotetezera; natengeko mwazi wa ng'ombeyo, ndi mwazi wa mbuziyo, ndi kuupaka pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira.

19. Ndipo awazepo mwazi wina ndi cala cace kasanu ndi katatu; ndi kuliyeretsa ndi kulipatula kulicotsera zodetsa za ana a Israyeli.

20. Ndipo atatha kucitira cotetezera malo opatulika, ndi cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, abwere nayo mbuzi yamoyo;

21. ndipo Aroni aike manja ace onse awiri pamutu pa mbuzi yamoyo, ndi kubvomereza pa iyo mphulupulu zonse za ana a Israyeli, ndi zolakwa zao zonse, monga mwa zocimwa zao zonse; naike izi pamutu pa mbuziyo, ndi kuitumiza kucipululu ndi dzanja la munthu wompangiratu,

22. ndi mbuziyo isenze yokha mphulupulu zonsezo kumka nazo ku dziko la pa lokha; ndipo azitaya mbuziyo m'cipululu.

23. Pamenepo Aroni alowe m'cihema cokomanako, nabvule zobvala zabafuta zimene anazibvala polowa m'malo opatulika, nazisiye komweko.

24. Ndipo asambe thupi lace ndi madzi kumalo kopatulika, nabvale zobvala zace, naturuke, napereke nsembe yopsereza yace, ndi nsembe yopsereza ya anthu, nacite codzitetezera yekha ndi anthu.

25. Ndipo atenthe mafuta a nsembe yaucimo pa guwa la nsembe.

26. Ndipo iye amene anacotsa mbuzi ipite kwa Azazeli atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

27. Koma ng'ombe ya nsembe yaucimo, ndi mbuzi ya nsembe yaucimo, zimene mwazi wao analowa nao kucita nao cotetezera m'malo opatulika, aturuke nazo kunja kwa cigono; natenthe ndi mota zikopa zao, ndi nyama zao, ndi cipwidza cao.

28. Ndi iye amene anazitentha atsuke zobvala zace, nasambe thupi lace ndi madzi, ndipo atatero alowenso kucigono.

Werengani mutu wathunthu Levitiko 16