nacitire cotetezera malo opatulika, cifukwa ca kudetsedwa kwa ana a Israyeli, ndi cifukwa ca zolakwa zao, monga mwa zocimwa zao zonse; nacitire cihema cokomanako momwemo, cakukhala nao pakati pa zodetsa zao.