Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Ezara 9:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zitatha izi tsono anandiyandikira akalonga, ndi kuti, Anthu a Israyeli, ndi ansembe, ndi Alevi, sanadzilekanitsa ndi anthu a maikowa, kunena za zonyansa zao za Akanani, Ahiti, Aperizi, Ayebusi, Aamoni, Amoabu, Aaigupto, ndi Aamori.

2. Pakuti anadzitengera okha ndi ana amuna ao ana akazi ao; nisokonezeka mbeu yopatulika ndi mitundu ya maikowa; inde dzanja la akalonga ndi olamulira linayamba kulakwa kumene.

3. Ndipo pakumva mau awa ndinang'amba cobvala canga, ndi maraya anga, ndi kumwetula tsitsi la pamutu panga ndi ndebvu zanga, ndi kukhala pansi m'kudabwa.

4. Nandisonkhanira ali yense wakunjenjemera pa mau a Mulungu wa Israyeli, cifukwa ca kulakwa kwa iwo a ndende; ndipo ndinakhala m'kudabwa mpaka nsembe yamadzulo.

5. Ndi pa nsembe yamadzulo ndinanyamuka m'kuzunzika kwanga, cobvala canga ndi maraya anga zong'ambika; ndipo ndinagwada ndi maondo anga, ndi kutambasula manja anga kwa Yehova Mulungu wanga;

6. ndipo ndinati, Mulungu wanga, ndigwa nkhope, ndi kucita manyazi kuweramutsa nkhope yanga kwa inu Mulungu wanga, popeza mphulupulu zathu zacuruka pamtu pathu, ndi kuparamula kwathu kwakula kufikira m'Mwamba.

7. Ciyambire masiku a makolo athu taparamula kwakukuru mpaka lero lino; ndi cifukwa ca mphulupulu zathu ife, mafumu athu, ndi ansembe athu, tinaperekedwa m'dzanja la mafumu a maikowo, kulupanga kundende, ndi kufunkhidwa, ndi kucitidwa manyazi pankhope pathu, monga lero lino.

8. Ndipo tsopano, kamphindi, Yehova Mulungu wathu wationetsa cisomo, kutisiyira cipulumutso, ndi kutipatsa ciciri m'malo mwace mopatulika; kuti Mulungu wathu atipenyetse m'maso mwathu, ndi kutitsitsimutsa pang'ono m'ukapolo wathu.

9. Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiya m'ukapolo wathu, natifikitsira cifundo pamaso pa mafumu a Perisiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wace, ndi kutipatsa linga m'Yuda ndi m'Yerusalemu.

10. Ndipo tsopano, Mulungu wathu, tidzanenanji pambuyo pa ici? pakuti tasiya malamulo anu,

Werengani mutu wathunthu Ezara 9